Psalms 79

Salimo la Asafu.

1Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowerera mʼcholowa chanu;
ayipitsa Nyumba yanu yoyera,
asandutsa Yerusalemu kukhala bwinja.
2Iwo anapereka mitembo ya atumiki anu
kwa mbalame zamlengalenga ngati chakudya,
matupi a oyera mtima anu kwa zirombo za dziko lapansi.
3Akhetsa magazi monga madzi
kuzungulira Yerusalemu yense,
ndipo palibe wina woti ayike mʼmanda anthu akufa.
4Ife ndife chinthu chonyozeka kwa anansi athu,
choseketsa ndi cholalatiridwa kwa iwo amene atizungulira.

5Mpaka liti Inu Yehova? Kodi mudzakwiya mpaka muyaya?
Kodi mpaka liti nsanje yanu idzayaka ngati moto?
6Khuthulirani ukali wanu pa anthu a mitundu ina
amene sakudziwani Inu,
pa maufumu
amene sayitana pa dzina lanu;
7pakuti iwo ameza Yakobo
ndi kuwononga dziko lawo.
8Musatilange chifukwa cha machimo a makolo athu
chifundo chanu chibwere msanga kukumana nafe,
pakuti tili ndi chosowa chachikulu.

9Tithandizeni Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu;
tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu
chifukwa cha dzina lanu.
10Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuti,
“Ali kuti Mulungu wawo?”
Ife tikuona, zidziwike pakati pa anthu a mitundu ina
kuti mumabwezera chilango chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa a atumiki anu.
11Kubuwula kwa anthu a mʼndende kufike pamaso panu;
ndi mphamvu ya dzanja lanu
muwasunge amene aweruzidwa kuti aphedwe.

12Mubwezere kwa anansi athu kasanu nʼkawiri
kunyoza kumene ananyoza Inu Ambuye.
13Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pabusa panu,
tidzakutamandani kwamuyaya,
kuchokera mʼbado ndi mʼbado
tidzafotokoza za matamando anu.
Copyright information for NyaCCL